Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 146
Miyambi ya Patsokwe
Choncho, tiyenera kuonetsetsa kuti tikuwachitira zabwino.
Chimodzimodzinso pantchito.
Mkamwini wankhuli adathira thendo la inswa pansanamira.
-Tiziyamba taonetsetsa tisananyanyale kuchita zinthu, chifukwa
nthawi zina tikanyanyala timataya zabwino.
Mkamwini waumbombo anakabisa mtolo wa mapira kumadzi.
-Tikakhala ndi zinthu ndi bwino kumagawirako ena chifukwa
tikapanda kutero zimawonongeka.
Mkanda wako ndi umene uli pakhosi.
-Timafunika kumakhutira ndi zomwe tili nazo.
Mkango ukazingwa umadya udzu.
-Ukakhala pamavuto susankha, kunyada umakusiya kaye apo,
n’kuyesetsa kuchita chilichonse kuti uthandizike.
Mkazi m’modzi diso limodzi, akazi awiri maso awiri.
-Munthu ukakhala pamitala sukhala pamavuto kwambiri ngati
mkazi m’modzi wamwalira. Mwambiwu umatanthauza kuti
ukakhala ndi podalira pawiri suvutika kwenikweni pamodzi pa-
kavuta.
Mkazi mmodzi ndi diso lopsinya.
-Si bwino kudalira chinthu chimodzi, chifukwa zikavuta
umasowa pogwira.
Mkazi ndi chitenje, chimathera pakhomo.
-Mkazi amayenera kukhala pakhomo n’kumasamalirapo bwino.
Mkazi si m’bale wako.
-Nthawi zambiri ukakwatira umakonda kwambiri mkazi wako.
Ena amafika pomanyoza achibale. Koma banja likatha limawa-
wasa kwambiri moti anthu ake amafika polakalaka wina at-
amwalira kuti asadzamuonenso. Chikondi chimatha banja lika-
tha.
145