Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 138
Miyambi ya Patsokwe
Mbalame ikakula siikhala paphira.
-Munthu wamkulu ayenera kukhala ndi khalidwe, monga mun-
thu wamkulu osati ngati mwana.
Mbalame ikatera pauta silasika.
-Kumakhala kovuta kuti uweruze mlandu wa m’bale wako mak-
amaka akapezeka kuti iyeyo ndi amene ali wolakwa.
Mbalame yagwa pa uta.
-Zinthu zavuta, zimakhala kuti zavuta basi.
Mbalame yakwawo ndi yakwawo, siiwala kwawo.
-Palibe angaiwale kwawo ngakhale kutakhala kutali bwanji.
Mbalame yamchira imamveka ikalira.
-Munthu waluso amadziwika ndi zimene amachita.
Mbalame zamthenga zofanana zimamwera chigoba chimodzi.
-Anthu ochita zofanana amayendera limodzi.
Mbalame zofanana nthenga zimayendera limodzi.
-Anthu ochita zofanana amayendera limodzi.
Mbalame zomwera chigoma chimodzi zimadziwana mthenga.
-Anthu a khalidwe lofanana amadziwana komanso kuchitira
zinthu limodzi.
Mbaliwali idabutsa chimoto.
-Zinthu zazing’ono zikhoza kuyambitsa mavuto aakulu ngati
mmene kamoto kakang’ono kamayambitsira chomoto chachiku-
lu n’kuotcha nkhalango yonse.
Mbawala siimwa madzi Galu ali kumbuyo.
-Munthu sangachite bwino chinthu, anthu ena akamamusowetsa
mtendere.
Mbawala yamantha idapota nyanga.
-Mantha amapulumutsa, umapewa mavuto omwe
137