Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 137
Miyambi ya Patsokwe
Mawu okweza ndawamva, am’munsi ndi nkhondo.
-Mawu abwino amawakweza, oipa amawang’ung’udza kuti ena
asamve.
Mawu osiyiza adaombola Kalulu.
-Nthawi zina anthu akatifunsa kuti tifotokoze nkhani tiyenera
kukamba nkhani modzigwira, osangonena chilichonse pokhapo-
kha ngati pakufunika kutero.
Mawu oswera mpanje (ng’oma) adautsa Fisi.
-Pakakhala mlandu ndi bwino kungonena zolakwazo, koma
ukayamba kufotokoza zidani zimene zinalipo kale, umatosa
zambiri.
Mawu oyamba anaphetsa Kalulu.
-Munthu ukafuna kuti umve zambiri umafunika kukhala woleza
mtima, osamangotengeka ndi zinthu zomwe sunazimvetse.
Mawu salawa, amalawa ndi chakudya.
-Osamayankhula moyerekeza ngati ukuwalawa kaye.
Mayankhayankha a pabwalo anatalikitsa Sakhwi mlomo.
-Poyankhula tizisamala, osamangochulukitsa mawu osafunika.
Mayendayenda amapha mapazi.
-Kuyendayenda kapena kuthamangathamana kumabweretsa
mavuto mwinanso imfa. Anthu amatha kumwalira chifukwa
mapazi awo anawatengera malo olakwika.
Mayendayenda amapha miyendo.
-Kuyendayenda kapena kuthamangathamanga kumabweretsa
mavuto nthawi zina.
Mbalame ikakhala pauta silasika.
-Zimakhala zovuta kuweruza mlandu wa m’bale wako.
136