Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 135
Miyambi ya Patsokwe
Mawere awirirana.
-Mawuwa amanenedwa ngati anthu apachibale sakugwirizana.
Mawere kapena kuti mabere amafunika kumakhala limodzi
pamtima, koma ngati atakula kwambiri amayamba kupaniki-
zana.
Mawonekedwe amapusitsa.
-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe pomwe si zokon-
gola kwenikweni.
Mawu a akulu amakoma akagonera.
-Mawu a akulu amakumbukiridwa pakapita nthawi ndiponso
pamene zomwe amanena zachitikadi.
Mawu a akulu amakoma akagonera.
-Mawu amene munthu wamkulu wanena amadzaoneka kuti
anali othandiza pakapita nthawi. Ndi bwino kumawatsatira.
Mawu a chitsiru amakoma akagonera.
-Mawu onenedwa ndi munthu wooneka ngati wopusa amadza-
khala othandiza m’tsogolo. Si bwino kumanyoza malangizo a
anthu ooneka monyozeka chifukwa nthawi zina amakhala
othandiza.
Mawu a munthu m’modzi ndi chisa cha njuchi.
-Ndi bwino kufunsa ena ukamva zinazake m’malo mofunsa
m’modzi chifukwa nthawi zina amangooneka okoma koma liri
bodza.
Mawu abwino saiwalika.
-Mawu oona samalephereka, amachitikadi. Komanso mawu
abwino, omwe munthu wanena amakumbukiridwa kwa nthawi
yaitali.
Mawu akuseri.
-Mawu achinsinsi. Anthu amanena mawu amenewa m’malo
134