Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 134
Miyambi ya Patsokwe
Matumbo a Nkhuku amafinyidwa paokha.
-Osamadzitama pagulu chifukwa tsiku lina zoipa zako
zimadzaululika n’kuipitsa mbiri yako yonse.
Matupa akumana.
-Anthu amakani okhaokha akakumana sakuna kugonjerana
pokhapokha wina awalanditse.
Maungu amafuwa pali moto.
-Amenewa ndi mawu amene anthu amanena mwana wa makolo
abwino akakhala wamakhalidwe oipa.
Maungu kubalira kumphuno.
-Mawawa amanenedwa munthu akamadandaula kuti zabwino
zabwera mochedwa.
Mavu anapangana kuning’a pamimba.
-Ndi bwino kumachita zinthu mogwirizana. Ngakhale kuti pan-
gano limavuta kusunga nthawi zina, komabe tiziyesetsa
kusunga zomwe tagwirizana popewa kukhumudwitsa ena.
Mavuto saona nkhope.
-Aliyense kaya ndi wabwino, wokongola kaya wotani, ama-
kumana ndi mavuto.
Mavuto sasowa.
-Kulikonse kumapezeka mavuto, palibe angawathawe.
Mavuto si maliro okha.
-Pali zinthu zina zomwe zimasowetsa mtendere kwambiri ngati
imfa, monga kusamvera kwa ana komanso zina.
Mawa ndi lero lomwe.
-Mwambiwu anthu amaunena popempha ngati kunena kuti ndi
bwino mungondibwereka chifukwa mawa ndi lero lomwe, si
kalekale.
133