Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 118
Miyambi ya Patsokwe
kuyambira limodzi ndi anzako.
Liwiro lilibe manyazi, chikakula patuka.
-Sitingathe kulimbana ndi Njovu ikakalipa. Tiyenera
kungothawa basi. Si bwino kumayesetsa kuchita zinthu zomwe
tikudziwa bwino kuti sizingatheke.
Lonjezo linadulitsa mutu wa Yohane.
-Uyenera kukwaniritsa zimene walonjeza.
Lungalunga mpobadwa, chilema chidza ku usana.
-Munthu ukhoza kulumala utakula kale. Munthu akhoza kubad-
wa ali bwinobwino n’kukhala ndi chilema atakula kale chifukwa
cha matenda kapena ngozi. Ungatanthauzenso kuti munthu
ukhoza kuyamba bwino koma pamapeto pake n’kusokoneza
zinthu.
Lungalunga mpobadwa, chilema chimadza utakula.
-Munthu ukhoza kulumala utakula kale. Ungatanthauzenso kuti
munthu ukhoza kuyamba bwino koma pamapeto pake
n’kusokoneza zinthu.
117