Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 117
Miyambi ya Patsokwe
Lero zakumana mbombo zokhazokha.
-Anthu a makhalidwe ofanana akakumana pamakhala mavuto,
palibe angapusitse mnzake.
Likawomba wotheratu.
-Mwayi ukapezeka, kapenanso ukakhala ndi nthawi, mpofunika
kuchitiratu zomwe ukufuna kuchita, chifukwa mwina tsiku
lotsatira kudzakhala mitambo. Si bwino kumachita zinthu
mochedwa mwayi ukapezeka. Ndi bwino kumachitiratu zinthu
mwayi ukadalipo.
Linda madzi apite, kenako uziti “ndadala.”
-Osamapupuluma kunena kuti zinthu zili bwino, chifukwa
pamapeto pake ukhoza kupusa utakumana ndi mavuto. Si
bwino kudzitama vuto lisanathe.
Linda mphepo iwombe kuti uone maliseche a Nkhuku.
-Pakagwa mavuto m’pamene umadziwa khalidwe lenileni la
mnzako.
Lirime ndi nkhondo.
-Mawu akhoza kuyambitsa nkhondo. Ndi bwino kumaganiza
kaye tisanayankhule kuopera kubweretsa mavuto titayankhula
zopanda nzeru.
Liuma lidakumbitsa Mbewa zapachulu.
-Nthawi zina makani amachititsa kuti uvutike kwambiri.
Mwachitsanzo, kuti munthu ukumbe mbewa zapachulu umafu-
nika kukhala ndi mphamvu. Ngati munthu ukufuna kuchita
chinthu monga kukumba mbewa zapachulu, uyenera kuchita
khama. Kusamva kungachititse kuti munthu akumbebe mbe-
wazi n’kukhaula.
Liwiro la mumchenga n’kuyambira limodzi.
-Ngati ukufuna kuti zinthu zikuyendere bwino, ndi bwino
116