Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 112
Miyambi ya Patsokwe
Kuyenda n’kuvina.
-Munthu ukakhala kwanu, si bwino kumachitira mwano alendo,
chifukwa tsiku lina ukayenda udzawapeza ndipo adzakuchitira
zoipanso. Munthu sudziwa kuti mawa ukapezeka kuti. N’zothe-
ka kufika kumene sumaganizira kuti ungafikeko.
Kuyenda ndi kuseri kwa phazi.
-Mawu onena kuti chinthuchi sindichikhulupirira kuti
chingachitike, koma chikadzachitika ndidzakhala ndi chim-
wemwe kwambiri.
Kuyenda usiku si kuona fisi.
-Kuyenda usiku ndi kuyenda ndi mdima waukulu, kunja kuli zii
ndi zoopsa zosiyanasiyana. Koma si kuti nthawi zonse amene
amayenda usiku amakumana ndi afisi.
Kuyenda utsi uli tsitu.
-Kuyenda ngati munthu wosazindikira.
Kuyera ndi madzi a nyemba.
-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe pomwe si zokon-
gola kwenikweni.
Kuyimba nthungululu pamaliro.
-Ngati munthu sukulongosola mbali yako pamlandu, anthu san-
gadziwe kuti ndiwe wosalakwa. Umakhala ngati ukuimba
nthungululu pamaliro zonse si zimene umafunika kuchita. Ngati
anthu akukuimba mlandu, umafunika kulira nkhawa zako
zonse.
Kuzima chinutu uzimba ukalipo.
-Chinutu ndi moto womwe alenje amayatsa pofuna
kuvumbulutsa nyama. Nthawi zina ndi bwino kumazimitsa mo-
towo chifukwa mawa mudzafunanso kusaka. Tiyenera kumasa-
mala ndi zinthu zomwe timagwiritsa ntchito. Komanso,
111