Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 111
Miyambi ya Patsokwe
kuphunzitsidwa kuyambira ali wam’ng’ono.
Kuyandikana si kuyanjana.
-Kudziwana si kukhala pamodzi ayi, koma kuyenderana.
Kuyasamula n’kupempha, mwana wa mfulu adziwa yekha.
-Kuyasamula n’kupempha mosafuna kuonetsera. Choncho,
munthu wachifundo amadziwa yekha chochita.
Kunyamula mpanda woola n'kuchulukana manja.
-Kuchitira zinthu limodzi komanso kuthandizana n'kofunika.
Kachepatsonga mtima ukunga phiri.
-Munthu wooneka monyozeka koma ali wanzeru komanso
wamphamvu kwambiri.
Kalowa m’nkhutu kalowa.
-Chimene munthu wamva wamva basi. Tizisamala poyankhula.
Kuyenda awiri si mantha.
-Anthu akakhala awiri amatha kuchita zinthu modalirana ndipo
amatha kuthandizana wina akapeza mavuto.
Kuyenda awiri si mantha.
-Anthu mukakhala pagulu mumathandizana komanso
mumalimbitsana mtima.
Kuyenda koma pamodzi.
-Anthu mukakhala pagulu mumathandizana komanso
mumalimbitsana mtima.
Kuyenda m’mawa n’kudya nawo.
-Munthu akafuna kugwira ntchito yake bwino amafunika ku-
lawira.
Kuyenda n’kupiringizika.
-Paulendo sungadziwe pomwe ukafikire.
110