Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 217

Matigari mosonyeza kuti zimene wanena Matigari zamumaliza kwabasi, ndipo ankangodziyerekezera iyeyo atadzikoleka zipolopolo, m’manja mwake muli mfuti. "Ayi," anatero Matigari. "Sindikufuna kuti mutaye miyoyo yanu masiku anu asanakwane. Tiyeni tisiyane pano. Ineyo ndipi- ta kukatenga zida zanga pansi pa mtengo. Kenako ndikatenga nyumba yanga mwamkokomo woopsa." "Chonde ndiloleni ndipite nawo," Guthera anatero. "Munthu amafa kamodzi basi, ndipo ndi bwino kufa ukuyesetsa kuchita zinthu zoyenera." "Inde. Ndife ana a Matigari ma Njiruungi," Muriuki anatero. "Ndife ana a anthu omenyera ufulu omwe anapulumuka nkhondo." "Komanso ndife azikazi awo!" anatero Guthera akumwetuli- ra. "Kodi ndi akazi ena ati omwe munkafunafuna?" Ndiyeno anakhala kaye chete. Kenako anayamba kuyakhula chapansipan- si zomwe zinkayendayenda m'mutu mwake. "Kungochokera pamene munandipulumutsa kwa galu uja, ndakhala ndikukhala moyo wosangalala. M'mbuyomu sind- inkasangalala ndi moyo umene ndinkakhala. Moyo wanga wonse ndinkangokhalira kumvera anthu enaake, atate wanga wakumwamba ndi atate wanga wapadziko lapansi. Komanso ndinkangokhalira kuponderezedwa ndi amuna, ansembe ko- manso amuna onse omwe ndinkachita nawo zauhule." "Ndikukutsimikizirani kuti m'mbuyo monsemu ndinkan- gochita zimene ena akufuna osati zimene ineyo ndasankha. Ndinkangokhala ngati ngolo yonyamula katundu wa eni ndipo ndinkachita zimenezi kaya ndikufuna kapena ayi. Ndinkango- khala moyo wosakhazikika komanso wosasangalala. 216