Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 216

Matigari ngakhale utanena mawu ozuna chamtundu wanji. Komanso si- kuti mdani angathamangitsidwe ndi zida zokha. Koma mawu a choonadi ndi chilungamo, akatengana ndi zida zankhondo, ukhoza kukwanitsadi kuthamangitsa mdani wako. Ngati chi- lungamo komanso mphamvu zili mbali imodzi, mdani wako an- gatsale wopanda kanthu! Ukakhala m'nkhalango yodzadza ndi zilombo zodya zinzake; mumsika woyendetsedwa ndi anthu akuba, zigawenga ndi akupha, chilungamo chimabwera ngati anthu omwe akuponderezedwawo agwirizana pamodzi n'kuyamba kulimbana ndi adani awowo ndi zida. Ndikulumbira chekecheke thwa! Boy sapitiriza kugona m'nyumba mwanga ngati ndingakhalebe ndi moyo! Ngati ndikunama mundikolowole disoli!" "Ndiye zinda zomenyera nkhondozo mukazitenga kuti?" Muriuki anafunsa. Matigari anayang'ana Guthera ndi Muriuki kwa kanthawi. Kenako anawauza nkhani ya mmene anatulukira m'nkhalango, atanyamula mfuti ya AK47, pistole, chikandalanga komanso lamba wam’chiuno wokolekapo zipolopolo. Anawauzanso kuti anabisa zida zakezi pansi pa mtengo wakachere. "Kodi mwambi uja umati chiyani? Munthu amabwerera ku- mene anachoka. Koma ndikufuna ndiuwonjezere. Munthu ama- bwerera n'kukamalizitsa nkhondo imene anaisiya. Ndifufuza mmene mapazi anga anadutsa kuti ndikayambirenso ulendo wanga kuchokera pamene ndinasiyiza. Ndikuona kuti ndi bwino timangenso nyumba ina limodzi. Nyumba yatsopano ya maziko olimba. Koma chomwe ndikudziwa n'choti, ngati nditapitirizabe kukhala ndi moyo, sindidzalola kuti Boy azigona m’nyumba imene ine ndinamanga." "Tiyeni tizipita! Tiyeni tipite kukatenga zida zanga!" Muriuki anayamba kuyankhula 215