Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 207
Matigari
Gawo 3
. . . Ino ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Pamene tikudikira
kumva zambiri zokhudza amisala amene athawa kuchipatala, talandira
nkhani yonena kuti boma la Britain komanso mayiko ena a ku ulaya
apereka ngongole kudziko lathu za mapaundi mamiliyoni ambiri kuti
athandize pa ntchito yoonetsetsa kuti m'dziko muno mukuchitika chi-
lungamo komanso kuti chilungamocho chiziperekedwa pompopompo.
Ndalamazi zigwiritsidwa ntchito kugula maunyolo, waya wamagetsi
woika pampanda wandende yemwe azithandiza kuti akaidi asamatha-
we, komanso zingwe zonyongera anthu amene aweruzidwa kuti
aphedwe. Zinthu zonsezi ziyenera kugulidwa m'makampani a ku Brit-
ain kapena m'mayiko omwe ali m'gulu la EEC. Ndalama zina zigwira
ntchito potumiza oyang'anira ndende, oweruza milandu m'makhoti
akuluakulu, apolisi olimbana ndi anthu achisokonezo komanso ab-
wanankubwa kuti apite kukaphunzira njira zatsopano zothandiza kuti
chilungamo chiziyenda bwino m'dziko muno komanso kuti
chiziperekedwa mwachangu. Nduna yoona zachilungamo yanena kuti
ikuyamikira kwambiri chifukwa cha ngongoleyi . . . Boma la United
States likupempha World Bank komanso IMF kuti libwereke dziko lino
ndalama zothandiza pachitukuko komanso zothandiza kuti malamulo
azitetezedwa n'kuonetsetsa kuti m'dziko muno mukuchitika chilunga-
mo chokhachokha . . .
Boma la United States lanenanso kuti likhoza kuthandiza dziko li-
no ngati litapempha ndege zapamwamba zankhondo, akasinja komanso
mahelokopita. Mneneri wa boma la US ndi amene ananena zimenezi
pamene anachititsa msonkhano. Anayamikiranso boma ladziko lino
pothandiza boma la USA pa nkhani za nkhondo m'mbali zonse . . .
206