Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 206
Matigari
Gawo 2
Nkhaniyo inadziwika koyamba cha m'ma 10 koloko m'mawa
ndipo inalengezedwa pa Wailesi ya Choonadi. Inanena kuti an-
thu openga angapo athawa kuchokera kuchipatala cha anthu
amisala.
Sizinkadziwika kuti athawa bwanji, koma apolisi ankaganiza
kuti n'kutheka anagwiritsa ntchito macheka podula waya
yemwe anazungulira chipatalacho.
Koma oyang'anira chipatalachi anadabwa kwambiri kuti od-
walawo anapeza bwanji machekawo chifukwa zinthu zonse
monga mitengo, malezala kapena chilichonse chakuthwa
sichinkaloledwa kulowa m'chipatalacho. Komanso ngakhale od-
walawo ankawadula zikhadaba. Ankachita zimenezi kuti od-
walawo asakhadzule anzawo milomo kapena kuwalemba nazo
anzawo kumaso.
Apolisi anapitiriza kufufuza nkhaniyi, ndipo inalengezedwa
pawailesi. Boma linachenjeza anthu kuti akhale osamala, chifu-
kwa ankaona kuti amisalawo ayenera ali ndi zida zomwe an-
gavulaze nazo anthu.
Komanso aliyense analimbikitsidwa kuti azimvetsera wailesi
chifukwa aposili apitirizabe kupereka malipoti a mmene nkhani-
yo ikuyendera. Ananena kuti wailesi iwauza amisalawo akag-
widwa.
205