Matigari
mwachitazi. Muzigona kutali ndi moto! Kodi simuomba m’man-
ja? Aa, tawaomberani m’manja akuluakuluwa kaya! Ombaninso!
Bola pamenepo! Mwawaona mapepala awa? Amenewa ndi
masheya. Masheyawa akupita kwa mtsogoleri wadziko lino,
Pulezidenti Ole. Koma pepala limodzili ndi langa, limenelinso
ndi la m asheya o m we and ipatsa. Dikirani kaye ndi malikhweru
komanso miluzi yanuyo. Muchita zimenezo mukamva zonse.
Kupereka masheya sikuti ndi nkhani yodabwitsa kwenikweni,
izi zimachitika ndithu. Pali makampani ambirimbiri omwe achi-
tapo zimenezi. Koma chosangalatsa kwambiri n’choti kampani
iyiyi yaperekanso masheya ena kuchipani cholamula. Kodi
mukudziwa tanthauzo la zimenezi?”
“Pajatu chipani cholamula ndi chathu. Ndi chipani cha ali-
yense wa ife. Ndi chipani chathuchathu. Choncho tinganene kuti
kampaniyi yapereka masheya kudziko lathuli, kwa tonsefe.
Kungoyambira lero, nonse kuphatikizapo amene sanakwanitse
kufika pamsonkhanowu, aliyense wa inu ali ndi masheya
kukampani imeneyi. Ndiyetu tinganene kuti kampaniyi ndi ya-
nunso. M’mawu ena, ndi ya tonsefe. Ndi kampani yadziko
lathu. Ilitu ndi boma labwino kwambiri, lomwe anthu onse ama-
khala eni ake akampani, kampani kukhala m’manja mwa ali-
yense! Ufulunso wodzilamulira pamenepo phi! Kodi sitinganene
kuti chimenechi ndiye chikomyunizimu cha ku Africa? Kodi
pangapezekenso ulamuliro woposa pamenepo amayi ndi abam-
bo? Chikomyunizimu chabwino ndi chimenechi, osati chija ama-
phunzitsa Karl Marx ndi Lenin, chomwe ophunzira komanso
aphunzitsi apenga nacho ngati chinayamba chawapatsapo nsi-
ma. Lak ini wato na cha m tem a k uni!*”
*Lakini watona cha mtema kuni (Kiswahili): Kutanthauza kuti, ‘anthu amenewa ti-
waonetsa polekera, tithana nawo.’
169