Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 169

Matigari “Munthu amene watsala kuti timugwire ndi amene akumadzitchula kuti Matigari ma Njiruungi. Koma ndikufuna kumuchenjeza munthu ameneyu. Dzanja la lamulo ndi lalitali kwambiri kuposa nsewu womwe wasankha keyendawu. Basi nkhani yamphekesera yabodzayi yathera pamenepa, ndipo is- amvekenso m’midza yonse ya kuno. Kunkhalango kulibenso anthu omenyera ufulu wadziko lino. Iwo anabwerera kalekale pamene tinalandira ufulu wathu n’kukweza mbendera yadziko lathu. Anthu amene anakana kubwerera, onse anawom- beredwa, full sto p*. Amene ali ndi makutu amve. Ndipo amene alibe akabwereke a mayi ake!” *Amenewa ndi mawu achingelezi omwe amanenedwa potsindika kuti palibenso zina zowonjezera. Zomwe zanenedwazo n’zokwanira. “Tsopano tiyeni tibwere kunkhani imene yandibweretsa kuno: Nkhani ya kusamvana pakati pa ogwira ntchito komanso oyendetsa fakitale ya Leather and Plastics. Ndisanapite patali, ndinauzidwa kuti pakhala kamwambo kenakake kapadera . . . ” Nthawi yomweyo Robert Williams komanso John Boy anad- zuka. Robert Williams anapereka cheke komanso mapepala enaake kwa John Boy. Nayenso John boy anapereka zinthuzo kwa nduna ija. Kenako anakhala pansi. “Choyamba ndiyamikire oyendetsa kampaniyi chifukwa cha ntchito yotamandika imene agwira. Mwachiona cheke ichi? Tachiyang’anani bwinobwino. Ife timafuna kumachita zinthu zonse poyera. Lino ndi dziko lachikhristu komanso timatsatira mfundo za demokalase ndipo timachita zonse moona mtima. Ichi ndi cheke cha 50,000 shillings ndipo chaperekedwa ku- thumba la apulezidenti lothandiza ana olumala. Kampani imen- eyi ili ndi anthu amtima wachifundo, achikondi komanso owolowa manja! Tathokoza kwambiri chifukwa cha zimene 168