Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 101
Matigari
M’mapolisi onse a m’tauni muno munadzadza. Anthu ena omwe
tinagwidwira limodzi awatsekera kupolisi ina, koma kungoti ku-
meneko malo anatha, n’chifukwa chake anandibweretsa kuno.
N’chifukwatu ndinakufunsani kuti: Kodi ndinudi Matigari ma
Njiruungi?”
“Inde, monga mmene wanenera, ndine amene,” Matigari
anayankha. Kenako anafunsa wogwira ntchitoyo, “Kodi ukudzi-
wa ngati Ngaruro wa Kiriro wamangidwa?”
“Sindikudziwa, koma ndamva apolisi akunena kuti akumu-
fufuza paliponse. Zikuoneka kuti anakwanitsa kuwazemba,”
wogwira ntchito uja anayankha.
“Kodi chilungamo chabisala pati m’dziko muno?” Matigari
anafunsa akukumbukira Ngaruro wa Kiriro komanso mmene
anamuthandizira masana a tsikulo.
“Ndiyankha funso limene mwafunsali,” munthu anaba nsima
uja anatero. “Musaganize kuti ndikukupeputsani kapena ku-
kuonerani m’botolo. Ndikufuna ndikuuzeni kuti mukapitiriza
kufunsa mafunso mukufunsawa, akupititsani kuchipatala cha
amisala kapena akakuponyerani m’dzenje lamdima wandiwey-
ani.”
“Dzenje lakuya kuposa limene tatsekeredwali?” wamowa uja
anafunsa. Kenako anatembenukira kwa Matigari. “Kuyambira
lero uzidziwika kuti Wofunafuna Choonadi ndi Chilungamo.
Mtima pansi! Mwana wa Mulungu anabatizidwa ndi Yohane
M’batizi. N’chifukwa chake ndatenga udindo wokubatizani
inuyo.”
“Choonadi kufunafuna Chilungamo?” Mlimi uja anananena
chapansipansi podabwa ndi zimene wamowa uja ananena.
“Chilungamo kufunafuna choonadi? Wofunafuna Choonadi ndi
Chilungamo!”
100