Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 100
Matigari
“Mawu a Ngaruro wa Kiriro anandisangalatsa kwambiri.
Nditaona kuti ziboliboli za Boy ndi Williams zikunyeka ndi mo-
to ndinamva bwino kwambiri mumtimamu moti ndimangokha-
la ngati ndaponda muufa. Ndinangotsala pang’ono kulira ndi
chisangalalo. Mwaona, ndakhala ndikugwira ntchito kwa zaka
zambiri pafalitale imeneyi. Ndinalipo kuchokera pamene oy-
endetsa kampaniyi anayamba kusintha. Poyamba kunabwera
Afalansa, kenako Ajeremani, Akanada ndiponso Aitale. Koma
sindinaonepo mabwana ovuta komanso ankhanza ngati Boy ndi
Williams. Ndipo Boy ndiye wanyanya kuvuta kwake moti ama-
posanso Williams. Ali ngati galu yemwe amauwa kwambiri
kuposa mbuye wake. Ndi wamwano komanso wodzimva. Ndi-
namvanso kuti amanena kuti tubzi take sitinunkha! Kodi ndi
ndani amene sangasangalale kuona anthu ankhanza ngati ame-
newa akukukuta mano ku Gehena? Mulungu wathu aticheukira.
Ndikukutsimikizirani, Mulungu wa ogwira ntchitofe aticheu-
kira.”
“Pamene ndimaganizira za Boy ndi Williams, ndinangoona
gulu la apolisi latizungulira. Munthu ndimacheza naye uja
ndinangomusiya n’kuthawa ndi mphamvu zanga zonse pog-
wiritsa ntchito miyendo yanga yokalambayi. Mwina mungafun-
se kuti kodi kameneka kanali koyamba kuthawa anthu atachita
sitiraka kuntchito? Ayi. Ndine katakwe pankhani yothawa zip-
wirikiti ngati zimenezi. Ogwira ntchitowo anangoti balalabalala
kuthawira mbali zosiyanasiyana. Apolisi komanso asilikali
anayamba kuwathamangitsa koopsa. Maso athu anangoti psu
ndi tsabola wa utsi wokhetsa misozi womwe apolisiwo ana-
phulitsa. Pamene ndimaponya mwendo kachitatu, kachinayi,
ndinangozindikira ndili m’manja. “Takugwira! N’chifukwa chi-
yani ukuthawa?” Posankhalitsa anandiponyera mu Land-Rover.
Mmenemotu ndi mmene zachitikira kuti ndipezeke kuno.
99