Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 3

Language Clarification Program: Kubwezeretsa zilembo zopanda liwu (consonants) m’malo omwe zilembo za liwu (vowels) zatsatana, zomwe malinga ndi malamulo a Chichewa ndi zosayenera. Bukuli ndi loyeserera pa nkhaniyi ndipo labwezeretsa chilembo cha “w” komanso cha “y” m’malo onse omwe chimafu- nikira kukhalapo, kupatulapo mawu ena apadera komanso obwerekera m’zinenero zina omwe samveka bwino akawonjezeredwa zilembozi. Zikuwoneka kuti chidule chowonongetsa zinthu n’chomwe chinachotsetsa zilembozi. Anthu anazolowera kulemba mwachidule chonchi moti sawona vuto zilembo za liwu kundondozana. Werengani bukuli kuti muwone mmene mawu a Chichewa amakongolera akalembedwa m’njira yolondolayi. Mfundo yofunika kuyiganizira ndi yakuti zolakwika sizisanduka zolondola kokha chifukwa choti anthu ambiri anazizolowera.