Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 60
Bonwell “Kadyankena” Rodgers
Seweroli linalembedwa cha m’ma 420 B.C.E., ndi mlembi wachigiriki
dzina lake Sofoko (Sophocles). Sofoko anabadwa m’chaka cha 495 B.C.E.,
ndipo anamwalira mu 405 B.C.E.
Edipa, yemwe anali mlendo ku Thebesi, anakhala mfumu atapha Mfu-
mu Layasi kukadali zaka 15 kapena 16 kuti zimene zili m’seweroli zichi-
tike. Iye anapatsidwa ufumuwu chifukwa anapulumutsa anthu a mu-
mzindawu kuchokera kwa chilombo china chomwe chinkadya anthu.
Edipa anapatsidwanso mkazi wa Layasi, dzina lake Yokasi ndipo anabe-
reka naye ana anayi; aamuna awiri, Utiko komanso Poliniko; komanso
awiri aakazi, Antigone ndi Isimene. Seweroli lamasuliridwa m’Chichewa
ndi Bonwell Kadyankena Rodgers.