Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 88
Paphata pa Chichewa
(2) Ndinadziwa kuti bambowa ndi akangandiwamba
nditawapezerera akumwa tiyi kubafa. (3) Amuna ena ndi
akangandiwamba, amachita kulemba zizindikiro mu ufa.
Kanjipiti: Munthu wamfupi kwambiri.
Chitsanzo: Ukakhala kanjipiti sukalamba mwansanga.
Umaona misana ya alangwani ikusanduka uta, iwe wako
uli gwa!
Kankha nthenga: Kutuma munthu.
Chitsanzo: Mpofunika kukankha nthenga kwa a mfumu.
Kankhira: Kunamizira munthu wina wosalakwa.
Chitsanzo: Sikutitu mundikankhire ine, nkhaniyi
sikundikhudza.
Kansanzawira: Munthu wovala nsanza.
Chitsanzo: Kukubwera a kansanzawira aja.
Kanthu n’chala: Kuti munthu udziwe bwino zinazake
pamafunika kuti ena akuuze bwinobwino.
Chitsanzo: Ndikufuna ndimvetsetse, pajatu kanthu
n’chala.
Kanthu ndi khama: Kuti upeze zimene ukufuna
umafunika kuchita khama.
Chitsanzo: Sinditopa kumufunsira mwina andilola. Paja
kanthu ndi khama, phwiti anakwatira njiwa.
Kanyama kanji: Mawuwa amanenedwa munthu akakhala
kuti sakudziwa za zinthu zinazake ndipo akufunsa kuti
adziwe zambiri.
Chitsanzo: Tabuleti ndi kanyama kanji?
Kanyanga nsambo: Kuimba bwino gitala.
Chitsanzo: Akati akanyange nsambo sungamudziwe.
87