Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 86

Paphata pa Chichewa Kamberembere: Munthu wodanitsa, munthu wosadalilika. Chitsanzo: (1) Pamudzi pano pachuluka akamberembere. (2) Akanadziwa kuti mwamuna wake uja ndi kamberembere sakanakwatira naye. Kambona: Munthu wolemera. Chitsanzo: Atsikana ambiri akumafuna kukwatiwa ndi kambona. Kamchacha: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Amene uja ndi kamchacha, safuna kuti matako ake akhale pansi. Kamkomya: Kuphikira mwamuna chakudya chomwe amachikonda, kusungira kapena kupereka chakudya kwa munthu amene umamukonda. Chitsanzo: (1) Ndikufuna ndikawapangile amunanga kam- komya. (2) Mkazi akakhala wamkomya, mwamuna sachoka pakhomo. Kamkonono: Wailesi yosamveka bwino. Chitsanzo: Tatseka kamkonono kakoko, tikugonatu ife! Kampalambutete: Munthu wometa mpala wa ngwee. Chitsanzo: Ukungodzivuta kupita kusukulu lero, aphunzitsi safuna kampalambutete. Kamthemba: Munthu wamtali komanso wamng’ono thupi. Chitsanzo: Kamthemba uja adakwatira mtsikana wamfupi zedi. Kamwendom’njira: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Kodi a kamwendom’njira aja alowera kuti? 85