Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 83
Paphata pa Chichewa
Kafumbu: Zinthu zambiri.
Chitsanzo: Chaka chino kuli kafumbu.
Kagwere uko: Choka pano. Mawuwa amasonyezanso kuti
munthuyo sukumufuna.
Chitsanzo: Atandiuza kuti amandifuna, ndinamuuza kuti
akagwere uko.
Kakaka: Kukamira, kusafuna kusintha maganizo.
Chitsanzo: (1) Mtsogoleri wachipembedzo uja
akulimbikitsa anthu kuti azikwatirana okhaokha pomwe
iyeyo ali kakaka ndi akazi ake. (2) Ukawauza zoti achite
amangoti kakaka pa maganizo awo.
Kakamula nkhani: Kuwonjezera zina ndi zina munkhani.
Chitsanzo: Osamakakamula nkhani, zikuvutanitu.
Kakumva kalemya: Mawuwa ndi ofanana ndi kunena
kuti, “ndikaona ndekha chifukwa kumvera kwa anthu ena
si kwabwino.”
Chitsanzo: Ndikaone ndekha, paja kakumva kalemya.
Kalamba:
(a) Kutha ntchito, kusiya kugwiritsidwa ntchito.
Chitsanzo: ChitsekoAnali kale awa, pano anakalamba.
(b) Kukhala wamkulu, wazaka zambiri.
Chitsanzo: Anali kale awa, pano anakalamba.
Kalambulabwalo: Woyamba kuchita zinthu ena
asanayambe, zochitika zoyambirira.
Chitsanzo: Angokhala akalambulabwalo awa, zenizeni
zikubwera.
Kalanga ine: Mawu amene anthu amanena ak-
amadandaula ndi zinazake kapena akamamva kupweteka.
82