Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 71

Paphata pa Chichewa Gwira chikho m’kati: Kuchimwa, kulakwa. Chitsanzo: Jemusi anagwira chikho m’kati. Gwira chiputu: Kana kuchoka. Chitsanzo: Akamuuza kuti achoke amangogwira chiputu. Gwira m’maso: Pusitsa. Chitsanzo: (a) Sindingalole kuti andigwire m’maso. (b) Kuteroko nawenso anakugwira m’maso? Gwira m’thupi: Menya. Chitsanzo: Amuna awo anawagwira m’thupi, n’chifukwa chake amalira. Gwira m’thupi: Menya. Chitsanzo: Amuna awo anawagwira m’thupi. Gwira mbuyo: Gwira matako. Chitsanzo: Mnyamatayo anamupatsa chibalo chopweteka chifukwa anagwira mbuyo ya mtsikana winawake. Gwira mphuno: Kupusitsa. Chitsanzo: Osamalola kuti anthu azikugwira mphuno. Gwira mpini: Kulima. Chitsanzo: Amene anagwira mpini chaka chatha, sanabwereko chimanjamanja. Gwira mwendo wachiwala: Khulupirira munthu wachabe. Chitsanzo: Muzisamala mukhoza kugwira mwendo wachiwala. Gwira njakata: Tanganidwa, kusowa chochita. Chitsanzo: Umagwira njakata mavuto akakupanikiza. 70