Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 67
Paphata pa Chichewa
sanadye nsima koma angodya zina.
Chitsanzo: Sitinadye, tangogonera mabanzi.
Gonera pamphumi: Kuchita zinthu mochedwa.
Chitsanzo: Ife tagonera pamphumi osadziwa kuti anzathu
akukatamuka ndi bizinezi ya nsomba.
Gontha m’kutu: Kusamva.
Chitsanzo: Munthu akamafuna kufa amayamba
n’kugontha m’kutu.
Gontham’kutu: Munthu wosamva. Tanthauzo lenileni la
dzinali ndi tizilombo touluka tofanana ndi ngumbi tomwe
timakhala tocheperapo.
Chitsanzo: Amene uja ndi gontham’kutu.
Gonthi: Munthu wosamvera. Mawuwa amatanthauzanso
munthu amene saamva mwachibadwa kapena chifukwa
cha matenda. Koma ndi oletsedwa ndi mabungwe oona za
ufulu kwa anthu olumala.
Chitsanzo: Mwanayu ndi gonthi.
Gudu: Munthu wolowerera za eni asanamvetse nkhani
yonse.
Chitsanzo: Inutu ndi gudu wogudukira zinthu za eni.
Mwamva kuti nkhaniyitu ikukukhudzani?
Gulidwa: Kuchitira munthu chinachake chifukwa
wakugwiritsa kenakake.
Chitsanzo: Apolisi ambiri amakhotetsa mlandu
akagulidwa. (2) Kodi wosewera ameneyu amugula eti,
n’chifukwa chiyani wadzichinya yekha?
Gulula mano: Menya modetsa nkhawa.
66