Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 61

Paphata pa Chichewa amfumu anawafula (anafulidwa). (b) Kuchotsa malesa a njuchi. Chitsanzo: Tikukafula uchi. (c) Kuunjika dothi kapena mchenga. Chitsanzo: Nkhululu zafula. Fulatira: (a) Kusiya kuyang’ana munthu mwadala. Chitsanzo: Nditawayang’ana, anandifulatira. (b) Kukunyanyala. Chitsanzo: Mulungu watifulatira. Fumbatitsa: (a) Kupatsa munthu ndalama. Chitsanzo: Ukagwira ntchitoyi ndikufumbatitsa kenakake. (b) Kugwiritsa chinachake m’manja. Chitsanzo: Kodi akufumbatitsa chiyani, ndalama? Fumbi lokhalokha: Anthu ambirimbiri. Chitsanzo: Kumaliroko kunali fumbi lokhalokha. Fumbi ndiwemwini: Mawuwa amatanthauza kuti nthawi zina ndi bwino kumanena zabwino zokhudza iwe mwini kuti zikuyendere. Angatanthauzenso kuti ngati ukufuna zikuyendere umafunika kulimbikira wekha. Chitsanzo: Ndinadziwa kuti akokomeza kwambiri zokhudza zimene amadziwa, paja fumbi ndiwemwini. Fumbi: Anthu ambiri, zinthu zambiri. Chitsanzo: Anthu omwe amawatsatira anali fumbi. Fumbwa: (a) Kudikira nthawi yaitali, kuchedwa. Chitsanzo: Anatidikiriritsa ife mpaka kufumbwa. 60