Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 59
Paphata pa Chichewa
Felemu ndi chitseko: Anthu ogwirizana kwambiri.
Chitsanzo: Anthu amenewa ndi felemu ndi chitseko.
Fera m’chipanda: Kumwa mowa moipa, kumwa mowa
kwambiri.
Chitsanzo: Malume anuwa adzafera m’chipanda.
Amakonda kumwa osadyera.
Fera m’mazira: Kutha zisanadziwike, kulephereka.
Chitsanzo: Boma linkati litipatsa chipukuta misozi, koma
zinangofera m’mazira.
Fera za eni: Kuzunzika pankhani za ena.
Chitsanzo: Analakwa ndi atsibweni anthu, ife tikungofera
za eni.
Finya munthu: Menya munthu, kwenya munthu
mwamphanvu.
Chitsanzo: Anzakewo anamufinya.
Fisi:
(a) Munthu wamantha.
Chitsanzo: Osamakhala ngati munthu wamkazi iyayi,
kumangochita mantha ndi chilichonse! Inutu ndi fisi.
(b) Munthu wankhuli (nkhwiru).
Chitsanzo: Pamudzi pano pachuluka afisi, amadya
chilichonse ndi apusi omwe, ndipo nyama ikaola sataya.
(c) Munthu amene ena amapeza kuti awaberekere mwana.
Chitsanzo: Inutu zakukanikani, mpofunika m’nyumbamu
tilowetsemo fisi.
Fodya wamkulu: Chamba.
Chitanzo: Ana ena a sukulu akumasuta fodya wamkulu.
58