Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 57
Paphata pa Chichewa
Dzina lodyera: Dzina longodzipatsa kuti anthu
azikudziwa mosavuta, dzina limene anthu amakudziwa
nalo ukamagwira ntchito kapena kuchita zinthu zina.
Chitsanzo: Dzina lawo lenileni ndi Masiye, limene
amadziwika nalo lija ndi dzina lodyera.
Dzinthu (vinthu): Chakudya chambiri.
Chitsanzo: Chaka chino tili ndi dzinthu (vinthu).
Dzionere wekha: Kuona ndi maso ako zimene
zikuchitika.
Chitsanzo: (1) Ndadzionera ndekha akulowa m’nyumba
ndi chibwenzi chawo. (2) Ndinapita komweko kuti
ndikadzionere ndekha.
Dzitho: Mphamvu.
Chitsanzo: Bamboyu ndi wadzitho.
Dzombe lidakapumula: Mawuwa amanenedwa pouza
munthu kuti azipita kwawo.
Chitsanzo: Pitani kwanu mudabwera lija ndi kale, dzombe
lidakapumula.
Dzukira kumanzere: Kusadzuka bwino, kudzuka moti
sungachedwe kukwiya kapena kupsa mtima.
Chitsanzo: Samala nawoni, adzukira kumanzere.
Dzulo laliwisiri: Dzulodzuloli.
Chitsanzo: Anabwera dzulo laliwisiri.
Dzungu m’gonera kumodzi: Munthu wokhala yekha.
Chitsanzo: Anthu ena amandichenjeza kuti ndidzaolera
m’nyumba chifukwa ndine dzungu m’gonera kumodzi.
Dzuwa kali tswii: Dzuwa likulowa.
Chitsanzo: Anabwera dzuwa lili tswii.
56