Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 52
Paphata pa Chichewa
ndi zikhulupiriro zachikuda, amaganiza kuti mwanayo
akhoza kudwala kapena kufa.
Chitsanzo: Amuna ambiri amapeza chibwenzi china akazi
awo akaima. Kenako zimadzapezeka kuti adula mwana
(asempha mwana).
Dula phazi: Kusiya kupitako.
Chitsanzo: Ankaona ngati ndimapita kwawo kuti
ndikadye, ndiye ndinangodula phazi.
Dula tsitsi ndi mano: Kusauka kwambiri.
Chitsanzo: Poyamba anali mpondamakwacha, lero
akudula tsitsi ndi mano.
Dula:
(a) Kunyada.
Chitsanzo: Mtsikanayu ndiye akudulatu masiku ano.
(b) Kukwera mtengo, kuvuta kupezeka.
Chitsanzo: Chimanga chikudula.
(c) Kuthamanga kwambiri.
Chitsanzo: Mwanayu amadula osati masewera.
(d) Kukhapa, kucheka kapena kugwetsa chinachake.
Chitsanzo: Dulani chingwechi.
Duli: Munthu wamakani.
Chitsanzo: (1) Mwanayu ndi duli. (2) Munthuyu ali ndi
uduli.
Dululu: Mankwala kapena chinthu chowawa kwambiri.
Chitsanzo: Chinangwa chake chinali dululu.
Dumbo: Nsanje, kaduka, kusirira koipa.
Chitsanzo: Mayi awa ali ndi dumbo.
Duwa: Mkazi wokongola.
51