Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 48

Paphata pa Chichewa Chotsa mano: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Osamawayamba dala anthu angadzakuchotseni mano. Chotsa ng’ala: Chenjeretsa kapena kukhaulitsa. Chitsanzo: Unachita bwino kumuchotsa ng’ala. Chucha: Kupusa Mwachitsanzo: Ana ochucha amakhala oti anawalerera pachilolo. Chulu cha ndiwo: Wooneka mopusa, munthu wopusa. Chitsanzo: Sindingalole kuti anthu ena azinditenga ngati chulu cha ndiwo. Chulukitsa ndi malovu: Kuwonjezera bodza. Chitsanzo: Zimene amanena zija wazichulukitsa ndi malovu. Chulutsa gaga m’diwa: Onjezera zonena. Chitsanzo: Ukamafotokoza nkhani, osamachulutsa gaga m’diwa chifukwa umangophimba mfundo zofunika. Chuma chimathawa: Chuma sichikhalitsa. Chitsanzo: Osamayerekedwa, kodi simudziwa kuti chuma chimathawa? Chuma chiyenda: Chuma sichikhalitsa. Chitsanzo: Osamayerekedwa, kodi simudziwa kuti chuma chiyenda? Chumba: Munthu wosabereka. Chitsanzo: Atakhala zaka ziwiri popanda mwana, mphekesera zinayamba kumveka kuti ndi chumba. 47