Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 46

Paphata pa Chichewa Chobwerera mbuyo: Kumayankhula nkhani ngati sukuidziwa. Chitsanzo: Munthu sayenera kumayankhula chobwerera m’mbuyo. Chocholoka: Chenjeretsa. Chitsanzo: Ana anuwa ndi ochocholoka. Choka mchere: (a) Kusakhalanso wachikoka. Chitsanzo: Kukongola si kanthu koma khalidwe. Umafunika kusankha munthu woti akadzachoka mchere, uzidzamukondabe. (b) Mkazi wosachita manyazi ndi amuna kapena mwamuna wosachita manyazi ndi akazi. Chitsanzo: Anthu anasiya kumufunsira chifukwa sakana munthu. Anachoka mchere. Choka penti: Kusiya kukongola. Angatanthauzenso kutha kapena kusukuluka. Chitsanzo: (a) Simunkagwirika mukuwala inu. Lero mwachoka penti ndiye mwatifuna. (b) Anali asungwana awa, koma lero achoka penti. Chokhetsa dovu: Chakudya chokoma kwambiri. Chitsanzo: Azakhali anatiphikira chakudya chokhetsa dovu. Chokhetsa malovu m’kamwa (chokhetsa dovu): Chakudya chokoma kwambiri. Chitsanzo: Azakhali anatiphikira chakudya chokhetsa malovu m’kamwa. Chokocha: Chotsa. Chitsanzo: Kampani ikufuna kuchokocha antchito ena. 45