Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 408

Paphata pa Chichewa Zwazwada: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Anamuuza kuti akakumana nayenso amuzwazwada. Zweta: Kuchita misala. Chitsanzo: Usamachite zinthu ngati wozweta. Zyoli: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Zitaululika kuti anaba chimanga ndi iwowo, anangoti zyoli. Zyolizyoli: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Zitaululika kuti anaba ufawo ndi iwowo, anayamba kuyenda zyolizyoli. 407