Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 403

Paphata pa Chichewa Zododometsa: (a) Zodabwitsa. Chitsanzo: Amachita zinthu zododometsa. (b) Kusokoneza. Chitsanzo: Amandidodometsa ndi amene anakhala pambuyo panga uja. Zoduka mutu: Zopanda nzeru. Chitsanzo: Zimene akunenazi ndi zoduka mutu. Zofooka: Zimene munthu amalakwitsa kapena sachita bwino. Chitsanzo: Ndikulimbana ndi zofooka zanga. Zogwira mtima: Zomveka bwino, zofika pamtima. Chitsanzo: Chitsanzo chimene wafotokozachi ndi chogwira mtima. Zoimitsa mitu: Zosokoneza maganizo. Chitsanzo: Zimene andiuza ndi zoimitsa mutu. Zokhudza mtima: Zomvetsa chisoni, zomveka bwino. Chitsanzo: Nkhaniyi ndi yokhudza mtima. Zokodola nseko: Zokupangitsa, zochititsa kuti munthu aseke. Chitsanzo: Amakamba nkhani zokodola nseko. Zokunkha: Zopeza movutikira, zochepa. Chitsanzo: Zakudya zomwe akumapeza ndi zokunkha. Zolaula: Mavidiyo, nkhani kapena zinthunzi zoonetsa maliseche. Chitsanzo: Mwanayu amaonera zolaula. Zomola: Kuchotsa ubweya kapena udzu mopanda dongosolo. Chitsanzo: Nkhukuyo angoizomolazomola basi. Zonda: (a) Kukaona kuti anthu ali bwanji Chitsanzo: Kodi munakawazondako amene akudwala aja. 402