Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 400
Paphata pa Chichewa
Zikuyenda? Zili bwino.
Chitsanzo: Ife zili bwino, kaya anzathu bwanji, zikuyenda?
Zilope: Mawuwa amanena za munthu amene akuchita
zinthu mwamphamvu kwambiri ndipo sakufuna kusiya.
Chitsanzo: Amagwira ntchito ngati ali ndi zilope.
Zilubwelubwe: Kuona zinthu zomwe palibe.
Chitsanzo: Nditangodzuka ndimaona zilubwelubwe.
Zilumika:
(a) Zaka.
Chitsanzo: Papita zilumika zambiri chilandilireni ufulu.
(b) Mawuwa amanenedwanso mokokomeza ponena za
chinthu chikachedwa.
Chitsanzo: Amati akapita kunsika amatengako zilumika.
Zimandifikapo: Zimandisangalatsa kwambiri.
Chitsanzo: Nyimbo zachikondi zimandifikapo.
Zimbaitsa: Kunena mokuluwika, kunyalanyaza kunena
mfundo yeniyeni.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani akunena mozimbaitsa.
Zimbwatha:
(a) Nkhuku ya miyendo yaifupi.
Chitsanzo: Sindikufuna kuweta azimbwatha.
(b) Munthu wamfupi.
Chitsanzo: Abale ake onse ndi azimbwatha.
Zimbwazimbwa: Saonekanso bwino.
Chitsanzo: Poyamba ankatchena, koma pano amangoti
zimbwazimbwa.
Zina kambu zina leku: Ndi bwino kumaona zoyenera
kunena m’malo momangoyankhula zilizonse.
Chitsanzo: Zina kambu zina leku, mwanayu akuchita
bwino zedi!
Zinamwa njuchi: Mwamuna wosabereka.
Chitsanzo: Bambowatu alibe mwana, zinamwa njuchi.
399