Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 395

Paphata pa Chichewa Zachilendo: Zodabwitsa. Chitsanzo: Ayamba kuchita zachilendo. Zachisawawa: (a) Zopanda dongosolo,. Chitsanzo: M’tauni mukungochitika zachisawawa. (b) Zongopezeka paliponse. Chitsanzo: Zinthu zimenezi sizimapezeka mwachisawawa. Zada: Zavuta. Chitsanzo: (1) Apa ndiye zanga zada. (2) Apa ndiye zinthu zamudera. Zagwa m’mbale: Zakhala bwino. Chitsanzo: Ndimafuna ndalama yogulira nsapato. Kenako amalume anandipatsa zawo moti zinagwa m’mbale. Zagwa ndi khope: Kukhala ndi zinthu zambiri mosayembekezeka. Chitsanzo: Zakudyazi zagwa ndi khope. Zagwa zatha: Zachitika basi, tingolimba nazo. Chitsanzo: Ngakhale mulire palibe chitasinthe, zagwa zatha basi. Zagwazatha: Munthu wolimba mtima. Chitsanzo: Iye ujatu ndi zagwazatha, kaya akumane ndi mavuto otani, sabwerera m’mbuyo. Zakeyu: Mawu achipongwe onenza za munthu wamfupi. Chitsanzo: Anangoona kukhala Zakeyu, koma mumtima mwakemo ndi wamtali. Zakumanja: Zochepa. Chitsanzo: Chaka chino angokolola zakumanja. Zakupsa: Zinthu zanzeru, zomveka, zaphindu komanso zoona. Chitsanzo: Zimene amayankhula zimakhala zakupsa zokhazokha. 394