Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 393

Paphata pa Chichewa Yendana pamsolo (pamutu): Kudererana. Chitsanzo: Anthuwa amayendana pamsolo, bwanji tsiku lina adzangobandulana? Yendera kumbuyo: Kudzitama. Chitsanzo: Sindifuna kucheza nawo chifukwa akakhala amakonda kuyendera kumbuyo. Yendera kumsana: Nyada, nyang’wa. Chitsanzo: Anayamba kuyendera kumsana atangogula ng’ombe zija. Yepula: Kungodutsa pamwambamwamba, kutenga pang’ono. Chitsanzo: (1) Sanachotse maluwa onse, anangowayepula. (2) Mitanda yake amangoyepula. Yera m’maso: (a) Kuchenjeretsa, kusaona zotsatira zoopsa za zimene ukuchita. Chitsanzo: (1) Lerotu wayera m’maso, ukufuna kulira eti? (2) Wayera m’maso, wayamba kuzindikira. (b) Kuzindikira. Chitsanzo: Apa ndiye ndayera m’maso, kani zimayenda chonchi! Yeretsa m’maso: Kukubera kapena kuchenjeretsa munthu, kupusitsa. Chitsanzo: (1) Ndinadziwa kuti kupusa kumeneku amuyeretsa m’maso. (2) Usamalire chikwama chakochi anthu angakuyeretse m’maso. Yetsemula: Kuchira matenda aakulu. Chitsanzo: Bambo anagonekedwa kuchipatala aja ayetsemula. Yokhetsa thukuta: Ntchito yovuta kwambiri, yolemetsa. Chitsanzo: Ukaphunzira kwambiri, sugwira ntchito yokhetsa thukuta. 392