Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 378

Paphata pa Chichewa Waphula: Walemera. Chitsanzo: Anzanu aja anaphula. Waphunzo: Wamwano. Chitsanzo: Mtsikanayu ndi waphunzo, pamamwa pake pamangobulika mwano wokhawokha. Waponda mwala: Ali ndi podalira. Chitsanzo: Akuyankha mwamakani bwanji, mwinatu wap- onda mwala. Wapsa katope: Chenjerani kapena nthawi yatha. Chitsanzo: Wapsa katope, tiyeni tiyambepo kusosa. Wapsa phwetekere: Chenjerani. Chitsanzo: Wapsa phwetekere, wina asakuyeretseni m’maso. Wapsa ulendo: Ulendo watheka. Chitsanzo: Wapsa ulendo, ndinyamuka lero! Wapsa: Ali mmaluzi. Chitsanzo: Munthu uja wapsa, alibe kalikonse. Wathupi lakanyenya: Wonenepa. Amanenedwa poganizira kuti nyama zonenepa ndi zimene zimakhala bwino kuzipanga kanyenya. Chitsanzo: Musamalere ana ndi wailesi ya kanema, zimapangitsa kuti akhale ndi thupi lakanyenya. Watola chikwama: Walemera. Chitsanzo: Mwana uja watola chikwama. Watumidwa: Mawuwa amanenedwa winawake akamadabwa ndi zochita za munthu wina yemwe akuoneka kuti akufuna kumulakwitsa kapena kumutapa m’kamwa. Chitsanzo: Kodi ukundifunsiranji zimenezi? Watumidwa eti? Waula mavu: Kuwotcha chimanga (ena amati mondokwa kapena dowe). 377