Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 370

Paphata pa Chichewa Vala jekete: Kuuma kwa chakudya monga nsima. Chitsanzo: Tachedwa kudya nsimayi, taonani mpaka yavala jekete. Vala mdima: Kuchita zinthu momasuka chifukwa kuli mdima. Chitsanzo: Ena satha kuvina kukamawala, koma mdima ukakuta, amavina bwinobwino. Amamasuka akavala m’dima. Vala zilimbe: Kulimba nazo, kupirira. Chitsanzo: Valani zilimbe, mwakula mwatha! Valira nguwo ya kasenye: Kulimbikira kwambiri ntchito. Chitsanzo: Mvula yatsala pang’ono, mpofunika kuvala nguwo ya kasenye. Viika: Kulakwa polankhula. Chitsanzo: Apa ndiye mwaviikatu, mwayankhula ngati mwana. Viikana m’madzi: Putirana milandu. Chitsanzo: (1) Anthuwa aviikana m’madzi. (2) Mwana woshashalika amaviika m’madzi anthu akwawo. Vinira: Kalipira. Chitsanzo: Ukamumenya mwanayu, makolo ake akakuvinira. Voko: Mokhala ngati kulanda, mwamakani,. Chitsanzo: Anabwera kudzatenga katundu wawo mwavoko. Vomera moto: Kusachedwa kugwirira moto, kusachedwa kutentha. Chitsanzo: Mitengo iyi imavomera moto. Vulala: Tenga matenda. Chitsanzo: Ukapitiriza kuyenda mothamanga uvulala. Dziko lake siili. 369