Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 367
Paphata pa Chichewa
ndikuundwa pano. (2) Inutu muundwira pamzere pano!
Ung’onoung’ono: Zovala zothina zomwe zimasokedwa
ngati ulusi unawathewa.
Chitsanzo: Mnyamata asamavale ngati nkhalamba,
ayenera kumaphinza ung’onoung’ono!
Ungwiro: Kukhala munthu wosachimwa, kusalakwitsa
chilichonse.
Chitsanzo: Mkazi wangwiro ndani angam’peze?
Unikira: Thandiza munthu kuyambanso kuona bwino
zinthu, thandiza munthu wina nzeru.
Chitsanzo: Sindinabwere kudzakuuzani zochita,
ndimangofuna ndikuunikireni.
Unjirira:
(a) Kuzunguliridwa ndi anthu.
Chitsanzo: Anthu angomuunjirira.
(b) Kutolera zinyalala.
Chitsanzo: Amene saunjirira saotha nawo.
Unjiunji: Kubwera anthu ambiri nthawi imodzi, kuunjika-
na.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani anthu angoti unjiunji?
Unthama: Kunama.
Chitsanzo: Ine ndinkadziwa kuti akuunthama.
Unyinji: Anthu ambiri.
Chitsanzo: Kumowako kunali unyinji.
Unyizi: Ulesi.
Chitsanzo: Mwanayu ali ndi unyizi.
Unyizi: Ulesi.
Chitsanzo: Mwanayu ndi waunyizi.
Unyolo: Chipangizo chachitsulo chomwe apolisi
amamangira opalamula.
Chitsanzo: Anamukwidzinga ndi unyolo.
366