Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 365
Paphata pa Chichewa
Ukadyole: Woneneza ena kuti iyeyo akome.
Chitsanzo: Anthu ena amapita kwa amfumu n’kukachita
ukadyole kuti akome.
Ukamira mankhwala: Anthu ena omwe akudwala
amawiritsa mankhwala n’kutenga nsalu n’kudzifunditsa
nawo atayang’ana mankhwala owira aja mpaka atachita
thukuta.
Chitsanzo: Uukamire mankhwalawa ngati ukufuna ku-
chira.
Ukhalira zomwezo: Mawuwa amanenedwa munthu
akakhumudwa ndi zimene wina akunena. Nthawi zambiri
zimene winayo amachita zimakhala zoti n’zosathandiza.
Chitsanzo: Ukhalira zomwezo! Anzako akulimbikira ntchi-
to n’kumathandiza mabanja awo.
Ukufuna ndichite kukuvulira kuti ukhulupirire? Mawu-
wa amagwira ntchito munthu wina akamakaikira akuona
umboni womveka bwino. Angatanthauze ukufuna ndichite
chiyani kuti ukhulupirire?
Chitsanzo: Iwe ndi Thomasi Didimo, ukufuna ndichite ku-
kuvulira kuti ukhulupirire?
Ukumu: Mphamvu.
Chitsanzo: Ife tilibe ukumu wochita zimenezi.
Ulalo: Mlatho.
Chitsanzo: (1) Amene safuna kunyowa akadutse paulalo.
(2) Muzidutsa paulalo mungadzapite ndi madzi.
Ulaya: Europe.
Chitsanzo: Apira ku Ulaya.
Ulemu wogwada mgolosale: Ulemu wonyanyira, ulemu
wosaona malo.
Chitsanzo: Mwanayu ali ndi ulemu wogwada m’golosale.
Ulova: Kusowa ntchito yoti uzigwira makamaka yolem-
bedwa. Munthuyo amatchedwa lova.
Chitsanzo: Anawachotsa ntchito moti panopa ali paulova.
364