Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 362
Paphata pa Chichewa
Tsumba:
(a) Manyazi.
Chitsanzo: Mayiyo anadzuka pamalowo tsumba lili njo.
(b) Kumeta m’malimbu n’kusiya tsitsi pakati pa mutu
chakutsogolo.
Chitsanzo: Wametetsa tsumba.
Tswanya:
(a) Kuphwanya, kuswa, kunyenya.
Chitsanzo: Ndinamupempha kuti anditswanyire mtedza.
(b) Kumenya koopsa.
Chitsanzo: Anzake amutswanya koopsa.
(c) Kuvulaza.
Chitsanzo: Mwala wanditswanya.
Tukula khutu:
(a) Ulula pang’ono.
Chitsanzo: Ndikanadziwa kuti akupita kumudzi
ndikanamutukula khutu.
(b) Kumvetsera mwatcheru.
Chitsanzo: Aliyense watukula makutu kuti amve zimene
tikukambirana.
Tukumuka: Kudzikweza, kudzimva.
Chitsanzo: Ndinadziwa kuti ayamba kutukumuka.
Tukwanitsa: Wolongolola, mwana kapena munthu
wochititsa kuti ena azikunena.
Chitsanzo: Mwana uyu ndi wotukwanitsa, taonani ali
manja lende.
Tula nkhawa: Uza munthu wina mavuto ako kuti
akuthandize.
Chitsanzo: Ndikupita kukawatulira nkhawa zanga.
Tulira nkhwinya: Kubwezera cholakwa kwa wosalakwa.
Chitsanzo: Angokutulirani nkhwinya, ndinu wosalakwa.
361