Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 357
Paphata pa Chichewa
Toleza: Kutolatola zinthu zomwe zili pansi kaya munsewu
kapena malo enaake.
Chitsanzo: Amatoleza nsonga za mzimbe.
Tomera: Funsira ukwati.
Chitsanzo: (1) Mtsikanayu anatomeredwa kale. (2) Akufu-
na kutomera.
Tondovilo: Kupusa.
Chitsanzo: Zitaululika kuti akunama anangoti tondovilo!
Tong’ola maso: Tulutsa maso pamtunda.
Chitsanzo: Ndinawaona akutong’orena maso, n’kutheka
anauzana zinazake.
Tonthoza:
(a) Limbikitsa.
Chitsanzo: Amanditonthoza ndikakhala pamavuto.
(b) Kuthandiza munthu kusiya kulira.
Chitsanzo: Tamutonthozani mwanayo.
Topitopi: Kuledzera kofika pomalephera kuyenda bwinob-
wino.
Chitsanzo: Ndinakumana nawo ali topitopi.
Totobwa:
(a) Kudikirira mpaka kutopa, kupusitsidwa.
Chitsanzo: (1) Anandindikiriritsa mpaka kutotobwa. (2)
Anandipeza ndili totobwa.
(b) Kupusa.
Chitsanzo: Bamboyu ndi wototobwa.
Totokola: Kugulula, kuchotsa chinthu penapake.
Chitsanzo: Wakuba wawatotokolera malata onse.
Towatowa: Kutobwanyika, kufewa.
Chitsanzo: Tomato yense ali towatowa.
Tsakamira: Kuima malo enaake.
Chitsanzo: Pamene tinkachoka ku Lilongwe, Dafuleni
anatsakamira ku Dedza.
356