Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 355
Paphata pa Chichewa
Thupi lozuka: Thupi lofutukuka, munthu wathupi
lalikulu.
Chitsanzo: Mayi awo ali ndi thupi lozuka.
Thushula: Menya kwambiri, panda.
Chitsanzo: Anzake amuthushula.
Thyola bano: Kutha msinkhu, kuyamba kusamba kapena
kutulutsa umuna.
Chitsanzo: (1) Mwana ujatu wathyola bano chaka
chathachi. (2) Wayamba kuchita manyazi kwambiri,
ndikukhulupirira kuti wathyola bano.
Thyola khola: Kusiya mkazi wako n’kumakagona kapena
kukakwatira wina.
Chitsanzo: Bambo aja anathyola khola n’kupita m’mudzi
wapamtundapo.
Thyola m’nkhongono: Kutha mphamvu
Chitsanzo: Sindinayembekezere kumva zimenezi moti
mwandithyola m’nkhongono.
Thyola mtima: Kukhumudwa.
Chitsanzo: Zimene achitazi zandithyola mtima.
Thyolera m’kamwa: Kudya.
Chitsanzo: Ndipatse bakhayu ndikathyolere m’kamwa.
Thyolera m’thumba: Ika ndalama m’thumba.
Chitsanzo: Atangolandira zake anazithyolera m’nthumba.
Thyolera:
(a) Kukhala wopirira.
Chitsanzo: Ngati ukufuna ukakhala bwino pamudzi
pamene paja, uzikangothyolera ngakhale akunyoze.
(b) Kugona.
Chitsanzo: Mlondayo anamupeza akuthyolera.
Thyoletsa bande: Thamangitsa.
Chitsanzo: Ukapitiriza kushashalika adzakuthyoletsa
bande.
354