Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 353
Paphata pa Chichewa
Thinana: Panikizana, zambiri.
Chitsanzo: (1) Akaidi amagona mothinana. (2) Akolola
chimanga chothinana.
Thipa: Munthu wonenepa.
Chitsanzo: Anakwatira thipa.
Thira dothi m’khutu: Kwirira munthu m’manda.
Chitsanzo: Chaka chatha n’chimene tidawathira dothi
m’khutu.
Thira m’dengu: Pusitsa.
Chitsanzo: Akungofuna kutithira m’dengu.
Thira mafuta: Pusitsa.
Chitsanzo: Ndinadziwa kuti akuthirani mafuta.
Thira mphepo: Kalipira.
Chitsanzo: Amachita chibwana. Lero amuthira mphepo.
Thira nkhondo: Kuika m’mavuto aakulu, kuukira ena.
Chitsanzo: Akuthirani nkhondo ndithu, mwawaputa dala.
Thiredopampu: Amenewa ndi mawu obwerekera ku-
chingerezi omwe pachichedwa amagwiritsidwa ntchito po-
nena mokokomeza za munthu amene amamwa kwambiri
tiyi kapena thobwa.
Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi thiredopampu.
Thokoza mapazi: Thawa zitavuta.
Chitsanzo: Azithokoza mapazi, akanamumenya.
Thomasi Didimo: Munthu wokayikira.
Chitsanzo: Iwe ndi Thomasi Didimo, ukufuna ndikuuze
bwanji kuti ukhulupirire?
Thotha: Thamangitha.
Chitsanzo: Ana onse awathotha.
Thothoka nsidze: Kupanda manyazi kapena mantha.
Chitsanzo: Sindifuna mtsikana wothothoka nsidze.
Thovu: Kulongolola.
Chitsanzo: Akamalankhula ndi anzake amachita thovu.
352