Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 351
Paphata pa Chichewa
Tenthatizime: Munthu woyambanitsa anthu.
Chitsanzo: Pamudzi pano pali tenthatizime.
Tepatepa: Kupanda mphamvu, kutalika kwambiri.
Chitsanzo: Akamayenda amangoti tepatepa.
Thabza mitambo: Kungochita zinazake pofuna kupusitsa
anthu kuti achoke, inuyo mukumanenso.
Chitsanzo: Titaona kuti pachuluka anthu, tinabalalika
mothabza mitambo. Timafuna enawo achoke kuti
tikumane tokhatokha.
Thamanga: Kugona ndi amuna kapena akazi ambiri.
Chitsanzo: (1) Mkazi amene uja ndi wothamanga. (2)
Wafatsa panopa, pakatipa anathamanga zedi mtsikana
ameneyu.
Thamangira kumatenda: Yendera odwala.
Chitsanzo: Ndikuthamangira kumatenda, amalume ad-
wala.
Thambitsa (thamba): Langidwa, theka.
Chitsanzo: Mpofunika kumuthambitsa mwana ameneyu.
Thambo: Dothi lakumanda.
Chitsanzo: Pofuna kukhaulitsa anamfedwa, adzukuluwo
anatenga thambo n’kukaliika kunsewu.
Thandala: Malo oyanikapo mbale. Nthawi zambiri
amamangidwa ndi mitengo.
Chitsanzo: (1) Ayanika mbale pathandala. (2) Tipange
thandala loyanikapo nsomba.
Thaphya: Kugona kapena kukhala pansi moti sungadzu-
kenso wekha.
Chitsanzo: Anamupeza ali thaphya, mowa uli m’mutu.
Thasathasa: Chophwamphwanthika, chafulati.
Chitsanzo: Chitumbuwa chimafunika kukhala
chathasathasa.
350