Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 348
Paphata pa Chichewa
Taya msuzi: Kutaya mbiri yabwino.
Chitsanzo: Ukalephera kudzigwira umatha kuchita zosay-
enera ndipo umataya msuzi wonse.
Tayale: Zili bwino.
Chitsanzo: Zithu zonse zili tayale.
Tayana: Lekana, dana.
Chitsanzo: Anthu ankagwirizana aja anatayana.
Tchaina: Chosalimba.
Chilichonse masiku ano ndi cha tchaina.
Tchaye: Tiyi.
Chitsanzo: Apita kukamtini kukamwa tchaye.
Tchemba: Chitini kapena chinthu chimene anthu
amakodzeramo usiku akamaopa kutuluka panja.
Chitsanzo: Lero sanatulutse tchemba wake.
Tchera kumwezi: Kulephera, kutulukiridwa kuti umana-
ma. Mawuwa amanenedwa ukazindikira kuti munthu
amafuna kukupusitsa, ndiye wamutulukira.
Chitsanzo: Amaganiza kuti akadzimvetsa chisoni ndi-
wapatsa ndalama, atchera kumwezi.
Tchera: Kukukonzera chiwembu, kufuna kukukola.
Chitsanzo: Akufuna kunditchera kuti wolakwa ndikhale
ine.
Tchika: Bedi, chitanda, kama.
Chitsanzo: Wodwalayo anamuika patchika.
Tchimo: Kuchita zinthu zoipa.
Chitsanzo: Munthuyu wachita tchimo.
Tchingo: Mpanda.
Chitsanzo: Akumanga tchingo kuti tisamapiteko.
Tchipa:
(a) Kumangolola aliyense.
Chitsanzo: Atsikana ovuta uja anatchipa masiku ano.
347