Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 341
Paphata pa Chichewa
Sisitira bondo: Zengereza.
Chitsanzo: Ukasisitira bondo anzako atenga.
Siwa: Nyumba yamasiye.
Chitsanzo: Titapita kumaliroko, tinauzidwa kuti tikagone
ku siwa. Koma si nsikidzi tinazipeza kumenekozo!
Siya fumbi lili kobo: Thawa, yendetsa galimoto mofu-
lumira kwambiri.
Chitsanzo: Amayendetsa ngati waledzera, moti anangosiya
fumbi lili kobo!
Siya kafumbu: Mwalira.
Chitsanzo: Amalume awo asiya kafumbu.
Siya phazi: Usamakonde kuyankhulayankhula.
Chitsanzo: Nditayamba kubwebwetuka, anangondichenje-
za kuti: “Siya phazi, ukasiya pakamwa padzakutsata!”
Sizinthu (sikanthu): Chopanda ntchito, munthu
wachachabechabe.
Chitsanzo: Mayi amene aja sizinthu!
Soka mphasa: Kugona chifukwa cha matenda.
Chitsanzo: (1) Masiku ano sakupeza bwino,
akumangosoka mphasa. (2) Sabata imeneyi ndimasoka
mphasa.
Sokolotsa:
(a) Vumbulutsa, thamangitsa.
Chitsanzo: Onse amene anabisala awasokolotsapo.
(b) Angatanthauzenso chimene chachititsa munthu
kuchoka kwinakwake.
Chitsanzo: Chakusokolotsani m’taunimo n’chiyani?
Sokoneza mutu: Kubalalitsa, kukupangitsa kuti usowe
chochita.
Chitsanzo: Nkhaniyi yandisokoneza mutu.
Solola mulomo: Kutsonya.
Chitsanzo: Ndinadziwa kuti akazi awo akwiya koopsa
chifukwa pamene amachoka anangosolola mulomo.
340