Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 333
Paphata pa Chichewa
Puma mwakathithi: Kumuma mwamphamvu, mosale-
keza.
Chitsanzo: Anatipeza akupuma mwakathithi, mwina zilipo
zoopsa zimene anaona, apo ayi ndiye kuti amamuthaman-
gitsa.
Pumitsa mapazi: Kusiya kuyenda wapansi, kuyenda pa-
galimoto kapena njinga.
Chitsanzo: Ndagula njinga kuti ndipumitseko mapazi.
Punduka: Wopuwala, yemwe ali ndi chiwalo chomwe chili
ndi vuto, mwina kupindika kapena kuduka. Mawuwa ndi
oletsedwa ndi mabungwe oona za ufulu wa anthu.
Chitsanzo: Ndikumenyera ufulu wa anthu opunduka.
Punzipunzi: Kudzilimbitsa kuti usagwe ukamamenyedwa
kapena ukamayenda modzikoka.
Chitsanzo: Ndinawaona ali punzipunzi kulowera kumsika.
Puta tsoka: Kudzibweretsera tsoka kapena mavuto.
Chitsanzo: Zoona angatukwane munthu wosalakwa uja,
kuliputatu tsoka kumeneko!
Puta: Palamula, kuyambana ndi munthu wina.
Chitsanzo: Wandiputa dala, ndimutibula. (2)
Akandiputanso ndimumenya.
Putira nkhondo: Kuika wina m’mavuto.
Chitsanzo: Ana anga mwandiputira nkhondo, bwanji
osakhuzumukako inu!
Puwaniza: Kuphwanya.
Chitsanzo: Apuwanizapuwaniza mango aja.
Puya madyedwe: Kudya zambiri kuposa mnzako.
Chitsanzo: Tikamapanga bulitsa, anthu ena amayambitsa
nkhani kuti awapuye anzawo madyedwe.
Pwamwantha: Menya modetsa nkhawa.
Chitsanzo: Munthu woyerekedwa uja anamupwamwantha
anzake.
332