Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 33
Paphata pa Chichewa
(b) Fungo lam’kamwa.
Chitsanzo: Mankhwala otsukira m’mano amachotsa
chifwirimbiti cham’kamwa.
Chigawenga:
(a) Munthu woipa mtima.
Chitsanzo: Nachonso ngakhale chigawenga chimapeza
mkazi woti chisungane naye.
(b) Katswiri.
Chitsanzo: (1) Mwana ameneyu ndi chigawenga cha
masamu. (2) Abusawa ndi chigawenga pa nkhani yodyetsa
mawu.
Chigendere: Amatanthauza chitsiru. Tanthauzo lake
silisiyana ndi la chibenga.
Chitsanzo: Amene uja anangoona kukula, koma ndi
chigendere.
Chigenga: Chitsiru
Chitsanzo: Kumalemekeza zigenga kuti upewe phokoso.
Chiimba chili m’mimba: Munthu ukakhala ndi njala
umalephera kuchita zinthu.
Chitsanzo: Ndikulephera ndi kuyankhula komwe, chiimba
chili m’mimba.
Chikandalanga: Chimpeni chachitali, chimpeni
chakuthwa konsekonse.
Chitsanzo: Akamapita m’malunje amanyamula
chikandalanga chake chija.
Chikhalamumthunzi: Malipiro omwe timalipira kwa
munthu asanayambe kuzenga mlandu. Mawu amenewa
amagwira ntchito pazochitika ngati, wina walanda mkazi
32