Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 322
Paphata pa Chichewa
Patelera: Pavuta.
Chitsanzo: Ataona kuti patelera, anangochokapo.
Pathala: Kusamba kwa akazi.
Chitsanzo: Palibe mkazi amene sakhala pathala.
Pathupi: Mayi amene watenga mimba, mayi wa pakati.
Chitsanzo: Akazi awo ali ndi pathupi.
Patsemtedzaupaone (ponyamtedzaupaone): Munthu
wandevu zambiri pakamwa komanso pachibwano pake.
Chitsanzo: Ndinakumana nawo dzulo. Bambo aketu ndi a
patsemtedzaupaone.
Patukana: Kusiya kukhalira limodzi kwa anthu omwe
anali pabanja.
Chitsanzo: Anthu akwatirana dzana aja apatukana.
Payera: Zatha.
Chitsanzo: Ndimafuna kukathyola misale, koma nditafika
ndinapeza payera.
Paza: Kungodutsa, kungoyenda.
Chitsanzo: Sindinabwere kudzakhazikika, ndikungopaza.
Pazamwala: Tambwali.
Chitsanzo: Aliyense amadziwa kuti amene uja ndi pa-
zamwala, palibe angamukongoze ndalama.
Pendapenda: Kusayenda bwino kwa zinthu. Mawuwa
amatanthauzanso kuyenda ngati ukufuna kugwa.
Chitsanzo: (1) Pakatipa zinthu zinali pendapenda. (2) Pen-
dapenda si kugwa koma kuchalira ulendo.
Penyera m’madzi: Yang’ana monyoza.
Chitsanzo: Anthu aja ayamba kupenyerana m’madzi.
Penyera patali: Kukhala ngati sakukuona.
Chitsanzo: Titafika kumudzi, sanabwere kudzatipatsa
moni moti amangotipenyera patali.
Penyerana m’kodi: Kudana.
Chitsanzo: Anyamata aja akupenyerana m’kodi.
321