Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 319

Paphata pa Chichewa Pakona: Pamavuto, zisakuyenda. Chitsanzo: Nthawi zambiri mwayi ngati umenewu uman- dipeza ndili pakona. Pakula ndalama: Kuba ndalama zambiri. Chitsanzo: Anthu ena a m’boma amapakula ndalama. Pala mano: Chenjeretsa. Chitsanzo: Ukapusa naye munthu ameneyu akupala mano. Pala moto kudambwe: Palamula. Chitsanzo: Pamenepatu wapala moto kudambwe. Palana ubwenzi: Kukhala paubwenzi, kugwirizana. Chitsanzo: Akufuna tipalane nawo ubwenzi. Palanga: Pala ndi mpeni ngati nyama yankhumba. Chitsanzo: Akupalanga nyama kuseriku. Palasika: Kalipira, kupsa mtima. Chitsanzo: Atamva zoti mwana wawo walephera mayeso, anayamba kupalasika. Palasira makala a moto: Kuika m’mavuto. Chitsanzo: Anthu oipa mtima ngati awa amakonda kupalasira anzawo makala a moto. Pali wina angati fwee apa! Pali wina angachite makani, pali wina anganditsutse. Chitsanzo: Ngati pali wina amene angati fwee abwere apa! Paliwombo: Pakati kapena pamwamba pa mutu. Chitsanzo: Mwanayu sanakhwime paliwombo. Pam’konda: Mvula yogwa mbali imodzi. Chitsanzo: Anadzikodzera poganiza kuti anyowabe ndi mvulayo. Koma anachita manyazi chifukwa mvula ya pamkondayo inangodutsa umo, n’kukata. Pamchenga: Kuphweka, kukhala chosavuta. Chitsanzo: (1) Timu imeneyi ndi pamchenga. (2) Mayeso ake anali pamchenga. 318